SIMBAZAKO/ ULENJE UMASIMBA WAKO

KUSINKHASINKHA ZA LAMULUNGU LA 8 PA CHAKA 

Introduction

We are called to lead others to Christ. We gather today before Christ to be energised by his Word and Sacraments. In his Word, we are implored to be kind in the way we speak and act towards others.  We all fall short and need purification, hence the need to use charitable words. 

Reflection points

Mphunzitsi (27:4-7) akuti zimene timayankhula zimaulula chenicheni chimene tili, zomwe zadzdza mumtima mwathu. Mwachitsanzo munthu wamatama ndi osavuta kumudziwa pokumva zoyankhula zake. Okummva zake zokha samasowa, ingomvetserani mukamacheza. Uthenga wabwinonso ukumaliza ndikuti “....pakamwa pa munthu pamalankhula zomwe zadzaza mumtima mwake.”

Muzoyankhula zathuzo tili ndi ufulu okamba zabwino zathu, inde kukometsa mbiri yathu. Koma sitiyenera kukometsa mbiri yathu poipitsa mbiri ya ena. Apa mchifukwa pali mau oti ülenje umasimba wako. Enanso ali dzina lawo ati Simbazako — dzina latanthauzo. Tikuziona mu Uthenga Wabwino.

Uthenga wabwino ukumveka ngati Ambuye Yesu akuletsa kuti tisamaloze zinthu zolakwika mwa ena. AYI ndithu. Zolakwikwa tizinene ndithu, tisadzisekere ndikumabisala pa mau awa kuti osaloza nzako chala. Tikatero tigwiritsa ntchito mauwa molakwika. Ena amatero kuti ansembe kudzudzulidwa zoipa e.g nthawi timava abale anthu andale amati ampingo musaloze zolakwika mundale chifukwa mumpingo mwanumo muli zakutizakuti. Inde zofookazo zilipo ndithu koma sizipangitsa kuti izo tikuloza zikhale zoyera kapena zovomerezeka. DOES IT MEAN I CANNOT POINT SOMETHING WRONG UNLESS I AM PERFECT MYSELF? SHALL I SHUT MY MOUTH & WATCH MY BROTHER GO ASTRAY OR SOME THINGS GOING BAD IN MY COMMUNITY simply because am not perfect? IMPOSSIBLE, I shall never be perfect after all. Chakwaipa tidane nacho osaleka kuchithawa, inde osaleka kuchikonza.

Inde tivomere kuti malangizo  amamveka bwino ngati operekayo akuyesetsa kukonza zake. Koma sikuti tidikire kuti tikhale opanda banga ndiye pamene tingakonze anzathu. We are our brothers keeper, kuthandizana, uku tikudziwa kuti nafenso tikuyenera kukonza mbali zina.

Ndie Ambuye Yesu amatanthauza chani apa “.....wonyengawe tayamba wachotsa chimtengo mmaso mwako....”. Background yamau awa ndi yakuti Ambuye Yesu aona mmene a Farisi amatsatira malamulo. Zabwino ndithu. Koma chifukwa chakusunga malamuwo amakhala ndimtima odzikhulupilira (sefl-righteousness), ndikumaona ena ngati ochimwa. Inde muja tichitira kuti anzathu ena kumawaona ngati akatolika a photocopy chifukwa sakwanitsa zimene ife timatha pachikhristu. Inde ija timati moral superiority.  Izi zimapagitsanso afarisi kuti aziiwala kuti nawo ali zolephera zao. Ndiye apa Yesu akuti...aaa polani moto afarisi. Musaonjeze, muli ndi zina zoti mukhonze mmoyo wanu, ndiye musayese mwayeleratu.

Ili ndi vuto lomwe timakhala nalo,,,pofuna kudziyeretsa pena timaipitsa ena. Kapena kungofuna kukwilira zathu zambiri ndiye timakokomeza za anzathu. Matenda amenewa tili nawo mmagulu mwathumu. Nthawi zina ena tangopanga ili kukhala khalidwe lathu...lokamba za ena ndipo zambiri zongofuna kuipitsa mbiri ya ena. Ambuye Yesu akuti, polani moto, simbani zanu kaye. 

Choncho nkhani yakula nsinkhu apa ndi yakuti mayankhulidwe athu asakhale odzidzikhulupilira udyo ndikumaona ena ngati okapsya, tipewe kukhala ma fault-finders, kumachita kuvalira magalasi kuti tione anzathu alakwitsa chani. Komanso tikafuna kudzudzula titero mothandiza mnzathuyo kuti asinthe. Ndi chifukwa pali mau amati tidane ndi cholakwa/tchimo osati olakwayo (condemn sin not the sinner), chifukwa atha kusintha. Ngati mukuyankhula za ena zikhale zowathandiza anzathuwo. 

AMBUYE MUNDIKONZE KUTI ZOKAMBA ZANGA ZIKHALE ZOMANGA UBALE, ZOTHANDIZA ANZANGA KUKHALA MOYO OSATI KUWAIKA MUNDENDE YAMUMTIMA, KAPENA KUWAPONYA KUDZALA. Amen. 

 — FM-